Pinned Tweet
Follow the Channel Africa Chinyanja channel on WhatsApp: whatsapp.com/channel/0029Vb8…
ChannelafricaNyanja retweeted
Bwelani mumve nkhani zabwino, zazikulu komanso zomveka bwino madzulo ano ndi Thamo Kapisa
#Zochitika | @Chinyanja1
ChannelafricaNyanja retweeted
Bwelani mumve nkhani zabwino, zazikulu komanso zomveka bwino madzulo ano ndi Thamo Kapisa
#Zochitika | @Chinyanja1
Yemwe anatsogolera chipani cha National Reconciliation Party for Unity and Prosperity -NRPUP pa masankho omwe anachitika ku Zambia mu mwezi wa August chaka chino, Brian Mundubile ndi yemwe anaima ngati wachiwiri wake Makebi Zulu, pamodzi ndi ena khumi ndi awiri,
2
31
tsapano awonekera mu bwalo lalikulu la milandu komwe akuyembekezeka kukana kapena kubvomeleza pa nkhani yofuna kuukira boma.
Oweruza milandu mu bwalo la Magistrate mu mzinda wa Lusaka, Chief Resident Magistrate Nthandise Chabala, ndiye watsindika Izi, kunena kuti walandira
2
Atsogoleri a maiko a Kenya ndi Democratic Republic of Congo, William Ruto ndi Felix Tshisekedi motsogozana, agwirizana za kufunika kugwira ntchito limodzi molemekezana pa kufuna kulimbikitsa ubale m'magawo osiyana siyana.
2
17
Atsogoleri awiriwa, agwirizana motere poona kuti ubale pakati pa maiko awiriwa unasokonekera chiyambireni mchaka cha 2023, pa nthawi yomwe dziko la DRC linadzudzula dziko la Kenya kuti likuikila kumbuyo gulu la zigawenga la M23 lomwe lakhala likulimbana ndi asilikali a boma
11
Adindo pa nkhani za ngozi zogwa mwa dzidzidzi ku Nigeria ati tsapano apeza matupi a anthu okwana 29 omwe amwalira pa ngozi ya kumira kwa bwato.
Izi ndi malingana ndi bungwe la National Emergency Management Agency lomwe lati anthuwa anali Pa ulendo opita ku maliro.
1
8
Nduna ya zachuma mdziko la Malawi a Joseph Mwanamvekha ati thumba la ndalama lomwe boma lasayinira ndi mayiko komanso nthambi zomwe zimathandizira dzikolo lithandizira kuti boma lichepetse mavuto akusowa kwa mafuta a galimoto.
3
27
Mkulu wa World Bank ku Malawi a Firas Raad ati dziko la Malawi lili ndi kuthekera kochita bwino ku nkhani za ndalama za kunja (forex) lomwe ndi vuto lalikulu pakadali pano ngati lingakhazikitse mfundo zabwino.
3
Dziko la Malawi lalandira thandizo la ndalama zokwana $221. 9 million zomwe zikuyembekezeka kugwiritsidwa ntchito zomwe mwa zina ndi za mtukula pakhomo komanso kulimbikitsa makampani kuti adzichita ntchito za malonda opititsa kunja.
7
Patadutsa miyezi yoposa isanu ndi umodzi chiyambireni pa nthawi yomwe matenda a Ebola anayamba kufalikira mdziko la DRC, akatswiri pa nkhani za sayansi akupitilira kuchita kafukufuku pa kufuna kumvetsetsa chomwe chikupangitsa kupitilira kofalikira kwa matendawa.
1
23
Dziko la Malawi, lasaina mgwirizano ndi dziko la Tanzania pa nkhani yotumiza odwala kukalandira thandizo kudzikolo. Maiko awiriwa asaina mgwirizanowu pa mwambo wapadera mu mzinda wa Dar es Salaam pomwe nduna za umoyo zati izi zithandiza a Malawi omwe akufunika thandizo lapadera.
1
37
Bungwe loona zipata mdziko la South Africa la Border Management Authority, lati nthambi pansi pa bungweli lotchedwa BMA Integrity Unit, lamanga anthu asanu omwe akuganiziridwa kuti akudzidwa pa mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu pa chipata cha Van Rooyens Gate.
1
33

